Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Anthu Osaona

Kuwonjezera Luso Lathu mu Utumiki​—Muzilalikira Anthu Osaona

KODI ZIMENEZI N’ZOFUNIKA BWANJI?: Anthu ambiri osaona samasuka kulankhula ndi anthu osawadziwa. Choncho kuti tilalikire anthu amenewa timafunika kuchita zinthu mwaluso. Yehova amakonda komanso kuganizira anthu osaona. (Le 19:14) Tingatengere chitsanzo chake ngati nafenso timayesetsa kuthandiza anthu osaona kuti akhale pa ubwenzi ndi Mulungu.

KODI TINGACHITE BWANJI ZIMENEZI?

  • “Muzifufuza anthu osaona.” (Mt 10:11) Kodi mukudziwa wina aliyense yemwe ali ndi wachibale wosaona? Kodi m’gawo lanu muli sukulu kapena bungwe limene limasunga anthu osaona omwe angakonde kumalandira mabuku athu?

  • Muzisonyeza kuti mumawaganizira. Anthu osaona amamasuka mukakhala aubwenzi komanso mukamasonyeza kuti mumawaganizira. Mungachite bwino kukambirana nawo nkhani zimene zingawachititse chidwi

  • Muziwapatsa mabuku athu. Pofuna kuthandiza anthu osaona komanso amene amavutika kuona, gulu la Yehova limatulutsa mabuku a zilembo za anthu osaona komanso zinthu zina zongomvetsera. Mungawafunse kuti angakonde kumaphunzira pogwiritsa ntchito njira iti? Woyang’anira utumiki ayenera kuonetsetsa kuti mtumiki wa mabuku akuitanitsa mabuku amene munthu wosaona akufuna.