Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 29-30

Yakobo Anakwatira

Yakobo Anakwatira

29:18-28

Yakobo sankadziwa kuti akumana ndi zotani pamene ankakwatira. Akazi ake, Rakele ndi Leya anayamba kulimbana. (Ge 29:32; 30:1, 8) Ngakhale m’banja lake munali mavuto, Yakobo ankaonabe kuti Yehova akumuthandiza. (Ge 30:29, 30, 43) M’kupita kwa nthawi ana ake anadzakhala mtundu wa Isiraeli.​—Ru 4:11.

Masiku ano, anthu omwe asankha kukwatira angakumanenso ndi mavuto. (1Ak 7:28) Komabe akhoza kukhala ndi banja labwino komanso losangalala ngati amadalira Yehova ndiponso kutsatira mfundo za m’Baibulo.​—Miy 3:5, 6; Aef 5:33.