Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

March 9-15

GENESIS 24

March 9-15

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

  • Vidiyo ya Ulendo Woyamba: (4 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: N’chifukwa chiyani tinganene kuti wofalitsayu wagwiritsa ntchito bwino mafunso? Kodi wofalitsayu anayankha zotani atamva zomwe mwininyumba ananena zokhudza Yesu?

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. (th phunziro 1)

  • Ulendo Woyamba: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 12)

  • Kuitanira Anthu ku Chikumbutso: (Osapitirira 3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha zimene tinganene poitanira anthu ku Chikumbutso. Wofalitsayo asonyeze chidwi. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti, Tizikumbukira Imfa ya Yesu kenako kambiranani naye mfundo za m’vidiyoyi. (th phunziro 11)

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

  • Nyimbo Na. 25

  • Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba Loweruka pa 14 March: (8 min.) Nkhani yokambirana. Perekani kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso kwa aliyense n’kukambirana mfundo zake. Onerani ndi kukambirana vidiyo ya zimene tinganene pogawira kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wanu wakonza kuti mudzathe kugawira timapepalati kwa anthu onse a m’gawo lanu.

  • Kodi Ndiitane Ndani?”: (7 min.) Nkhani yokambirana.

  • Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 76

  • Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (Osapitirira 3 min.)

  • Nyimbo Na. 115 ndi Pemphero