Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Ndiitane Ndani?

Kodi Ndiitane Ndani?

Chaka chilichonse timayesetsa kuitana anthu a m’gawo lathu kuti adzapezeke pa mwambo wa Chikumbutso. Ambiri mwa anthuwa sitiwadziwa. Komabe, tiyeneranso kumaitana anthu amene tikuwadziwa. Anthu amene amalandira kapepala kuchokera kwa anthu amene akuwadziwa, nthawi zambiri amabwera ku Chikumbutso. (yb08 11 ¶3; 14 ¶1) Kodi ndi anthu enanso ati omwe mungawaitane?

  • Achibale

  • Anzanu a kuntchito kapena a kusukulu

  • Oyandikana nawo nyumba

  • Maulendo anu obwereza, maphunziro anu komanso anthu omwe munkaphunzira nawo m’mbuyomo

Akulu akhozanso kuitana anthu omwe anafooka kuti abwere kumwambowu. Bwanji ngati munthu amene mumadziwana naye sakhala m’gawo la mpingo wanu? Mungamuthandize kudziwa nthawi ndi malo omwe kukachitikire mwambowo popita patsamba loyamba la webusaiti yathu pamene palembedwa kuti ZOKHUDZA IFEYO, n’kusankha pamene palembedwa kuti “Chikumbutso.” Pamene mukukonzekera Chikumbutso cha chaka chino, ganizirani za anthu amene mungawaitane kuti adzabwere pamwambowu.