Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Zimene Tinganene

Zimene Tinganene

●○○ ULENDO WOYAMBA

Funso: Kodi Yesu ndi ndani?

Lemba: Mt 16:16

Funso la Ulendo Wotsatira: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?

○●○ ULENDO WOBWEREZA WOYAMBA

Funso: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?

Lemba: Mt 20:28

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe imene Yesu anapereka?

○○● ULENDO WOBWEREZA WACHIWIRI

Funso: Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira nsembe imene Yesu anapereka?

Lemba: Yoh 17:3

Funso la Ulendo Wotsatira: Kodi pamisonkhano ya Mboni za Yehova pamachitika zotani?

NTCHITO YOITANIRA ANTHU KU CHIKUMBUTSO (14 March–7 April):

“Tikukuitanirani ku mwambo wofunika kwambiri womwe udzachitike padziko lonse. Mwambo umenewu ndi wokumbukira imfa ya Yesu.” Kenako m’patseni kapepala. “Kapepalaka kakusonyeza nthawi komanso malo omwe mwambowu udzachitikire m’dera lathu lino. Tikukuitananinso kuti mudzamvetsere nkhani yapadera yomwe idzakambidwe kumapeto a mlungu wa March 30.”

Funso la Ulendo Wotsatira Ngati Munthuyo Wasonyeza Chidwi: N’chifukwa chiyani Yesu anafa?