April 12-18
NUMERI 20-21
Nyimbo Na. 114 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Muziyesetsa Kukhalabe Ofatsa Mukapanikizika”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Nu 20:23-27—Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aroni anachita atalakwitsa zinthu komanso mmene Yehova ankamuonera ngakhale kuti analakwitsa zinthu zina? (w14 6/15 26 ¶12)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Nu 20:1-13 (th phunziro 2)
KUPHUNZITSA WALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 12)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. Mugawireni chimodzi mwa Zinthu Zophunzitsira. (th phunziro 3)
Nkhani: (5 min.) g 1/15 9—Mutu: Kodi Mungatani Kuti Muziugwira Mtima? (th phunziro 16)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muzilankhula Mawu “Olimbikitsa”: (7 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi kulankhula zosalimbikitsa komanso kukonda kudandaula kumakhudza bwanji ena? N’chiyani chinathandiza m’bale wa mu vidiyoyi kuti asinthe?
Musamangotengera Zochita za Anzanu: (8 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi anthu ambiri amakakamizidwa kuti achite zinthu ziti? Kodi palemba la Ekisodo 23:2 pali malangizo otani?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 129 ndi bokosi lakuti “Kukwapula”
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 13 ndi Pemphero