Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Muziyesetsa Kukhalabe Ofatsa Mukapanikizika

Muziyesetsa Kukhalabe Ofatsa Mukapanikizika

Mose, yemwe anali munthu wofatsa, anayesedwa pamene anapanikizika komanso anali ndi nkhawa (Nu 20:2-5; w19.02 12 ¶19)

Pa nthawi ina Mose analephera kukhalabe wofatsa ndipo anapsa mtima (Nu 20:10; w19.02 13 ¶20-21)

Yehova anapereka chilango kwa Mose ndi Aroni chifukwa cha zimene analakwitsa (Nu 20:12; w09 9/1 19 ¶5)

Munthu wofatsa sakwiya msanga komanso sakhala wonyada kapena wodzikuza. Anthu ena akamukhumudwitsa, amakhala woleza mtima, sakwiya, sasunga zifukwa komanso sakhala ndi mtima wofuna kubwezera.