Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri mu Utumiki

Mawu a Mulungu ndi amphamvu. (Ahe 4:12) Amafika pamtima anthu, ngakhale amene sadziwa Mulungu. (1At 1:9; 2:13) Timakhala ndi chimwemwe chodzadza tsaya tikaona munthu akusangalala ndi mfundo ya m’Baibulo yomwe tamusonyeza, imene kwa iyeyo ndi koyamba kuimva.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​—MUZIGWIRITSA NTCHITO MAWU A MULUNGU NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji Mawu a Mulungu pothandiza Jane kudziwa kuti ndi bwino kulola Mawu a Mulungu kuyankha mafunso athu?

  • Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji Mawu a Mulungu pouza Jane kuti awerenge lemba mokweza komanso potchula mfundo yaikulu ya lembalo?

  • N’chiyani chikusonyeza kuti lemba lomwe linawerengedwa linamufika pamtima Jane, nanga mukuganiza kuti Anita anamva bwanji?