Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzisankha Anzanu Mwanzeru

Muzisankha Anzanu Mwanzeru

Zimene zinachitikira Aisiraeli m’zigwa za Mowabu ndi chenjezo kwa Akhristufe. (1Ak 10:6, 8, 11) Aisiraeli amene anayamba kugwirizana ndi atsikana achimowabu, amene anali achiwerewere komanso ankalambira mafano, anachita machimo aakulu. Zimenezi zinabweretsa mavuto aakulu. (Nu 25:9) Nafenso tili ndi anzathu akuntchito, akusukulu, oyandikana nawo nyumba, achibale komanso anthu ena odziwana nawo amene salambira Yehova. Kodi tingaphunzire chiyani kuchokera pa nkhani ya m’Baibulo imeneyi zokhudza kuopsa kogwirizana ndi anthu ngati amenewa?

ONERANI MBALI YA VIDIYO YAKUTI ZITSANZO ZOTICHENJEZA MASIKU ANO, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi maganizo olakwika ati amene Zimiri ndi anthu ena anauza Yamini?

  • Kodi Pinihasi anathandiza bwanji Yamini kuti ayambe kuona zinthu moyenera?

  • Kodi pali kusiyana kotani pakati pa kukhala waubwenzi kwa munthu wosalambira Yehova ndi kukhala bwenzi la munthuyo?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala posankha anzathu apamtima ngakhale mumpingo?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kupewa magulu a pa intaneti ochezera a anthu amene sitiwadziwa?