Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Ine Ndine . . . Cholowa Chako”

“Ine Ndine . . . Cholowa Chako”

Yehova anapatsa ansembe ndi Alevi mwayi wapadera wochita utumiki wofunika kwambiri (Nu 18:6, 7)

Anthu a fuko la Levi sanalandire cholowa cha malo. Cholowa chawo anali Yehova (Nu 18:20, 24; w11 9/15 13 ¶9)

Aisiraeli ankapereka chakhumi pa zokolola zawo kuti chizithandiza Alevi ndi ansembe (Nu 18:21, 26, 27; w11 9/15 7 ¶4)

Yehova analonjeza Alevi ndi ansembe kuti aziwapatsa zofunika pa moyo. Sitiyenera kukayikira kuti Yehova adzatisamalira ngati titadzimana zinthu zina n’cholinga choti tizimutumikira.