Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso

Zimene Mungachite Kuti Muzisangalala Kwambiri Mu Utumiki​—Muzifunsa Mafunso

Yehova, yemwe ndi “Mulungu wachimwemwe,” amafuna kuti tizisangalala tikakhala mu utumiki. (1Ti 1:11) Timasangalala kwambiri tikamayesetsa kuwonjezera luso lathu lophunzitsa. Kufunsa mafunso kumachititsa kuti munthu akhale ndi chidwi komanso ndi njira yabwino yoyambira kucheza. Mafunso amathandizanso anthu kuganiza. (Mt 22:41-45) Tikafunsa munthu funso, n’kumamumvetsera pamene akuyankha, timakhala tikumuuza kuti ‘Ndinu ofunika kwa ine.’ (Yak 1:19) Zimene munthuyo wayankha zingatithandize kudziwa zoyenera kulankhula.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​MUZIFUNSA MAFUNSO  NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi makhalidwe abwino ati amene Jane anasonyeza?

  • Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji mafunso posonyeza kuti akuchita chidwi ndi Jane?

  • Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji mafunso pothandiza Jane kuti achite chidwi ndi uthenga wabwino?

  • Kodi Anita anagwiritsa ntchito bwanji mafunso pothandiza Jane kuganiza?