Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Musamatsanzire Anthu Amene Ndi Osakhulupirika

Musamatsanzire Anthu Amene Ndi Osakhulupirika

Kora, Datani ndi Abiramu anasonyeza kusamvera Yehova pogalukira dongosolo lake. Yehova anawononga anthuwa komanso ena amene anali kumbali yawo. (Nu 16:26, 27, 31-33) Kodi ndi zochitika ziti zimene zingayese kukhulupirika kwathu kwa Yehova? Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zingatithandize kuti tisamatsanzire anthu osakhulupirika?

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUSAMATSANZIRE ANTHU OSAKHULUPIRIKA NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Neliya anakumana ndi mayesero otani, nanga ndi chitsanzo chiti chimene chinamuthandiza kuti asonyeze kukhulupirika?

  • Kodi m’bale wina amene anakhumudwa anakumana ndi mayesero otani, nanga ndi chitsanzo chiti chomwe chinamuthandiza kuti asonyeze kukhulupirika?

  • Kodi M’bale Eliyoti anakumana ndi mayesero otani, nanga ndi chitsanzo chiti chimene chinamuthandiza kuti asonyeze kukhulupirika?

  • Kodi m’bale wina anakumana ndi mayesero otani kusukulu, nanga ndi chitsanzo chiti chimene chinamuthandiza kuti asonyeze kukhulupirika?