March 8-14
NUMERI 9–10
Nyimbo Na. 31 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Amatsogolera Anthu Ake”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
Nu 9:13—Kodi tikuphunzira chiyani pa malangizo amene Aisiraeli anapatsidwawa? (it-1 199 ¶3)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) Nu 10:17-36 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuitanira Anthu ku Chikumbutso: (3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene poitanira anthu ku Chikumbutso. Pambuyo poti mwininyumba wasonyeza chidwi, yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti, Tizikumbukira Imfa ya Yesu kenako kambiranani naye mfundo za m’vidiyoyi. (th phunziro 11)
Ulendo Wobwereza: (3 min.) Itanirani ku Chikumbutso mnzanu wakuntchito kapena wakusukulu amene munamulalikirapo m’mbuyomu. (th phunziro 2)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) bhs 214, Mawu Akumapeto 16. Muitanireni ku Chikumbutso ndipo mufotokozereni kuchokera m’Baibulo chifukwa chake sayenera kukadya zizindikiro. (th phunziro 17)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kusintha Zinthu pa Beteli Kukuthandiza pa Ntchito Yolalikira: (10 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa: Kodi pamsonkhano wapachaka wa 2015 panaperekedwa chilengezo chotani, nanga ndi zifukwa ziwiri ziti zomwe zinachititsa kuti pakhale kusintha? Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zinasintha pa Beteli, ndipo kusinthaku kwathandiza bwanji? Kodi chilengezochi chinakhudza bwanji ntchito yosamutsa nthambi ya ku Britain? Kodi kusintha kumeneku kukusonyeza bwanji kuti Yehova akutitsogolera?
Chimene Tinabwerera ku Beteli: (5 min.) Onerani vidiyoyi.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 124
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 113 ndi Pemphero