Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Mavuto Onse Ali Ndi Tsiku Lothera

Mavuto Onse Ali Ndi Tsiku Lothera

Mavuto akhoza kutifooketsa, makamaka ngati atenga nthawi yaitali. Davide ankadziwa kuti mavuto amene ankakumana nawo kuchokera kwa Mfumu Sauli adzatha, ndipo adzakhala mfumu monga mmene Yehova analonjezera. (1Sa 16:13) Chikhulupiriro chinamuthandiza Davide kuti akhale woleza mtima n’kumayembekezera Yehova.

Tikamakumana ndi mavuto, tikhoza kuchita zinthu mochenjera, mwanzeru komanso tingagwiritse ntchito luso lathu la kuganiza kuti tithane ndi mavuto amene tikukumana nawowo. (1Sa 21:12-14; Miy 1:4) Komabe, mavuto ena sangathe ngakhale titachita zinthu zonse zimene tingakwanitse zomwe ndi zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Pa zochitika ngati zimenezi tiyenera kukhala oleza mtima n’kumayembekezera Yehova. Posachedwapa, iye athetsa mavuto onse ndipo ‘apukuta misozi yonse’ m’maso mwathu. (Chv 21:4) Kaya mavuto athu atha chifukwa choti Yehova walowererapo, kapena pa zifukwa zina, mfundo yosatsutsika ndi imodzi: Mavuto onse ali ndi tsiku lothera. Imeneyitu ndi mfundo yolimbikitsa kwambiri.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ANTHU OGWIRIZANA M’DZIKO LIMENE ANTHU AKE SAGWIRIZANA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi ndi mavuto otani omwe Akhristu a kummwera kwa United States ankakumana nawo?

  • Kodi anasonyeza bwanji kuleza mtima komanso chikondi?

  • Kodi anatani kuti aike maganizo awo onse pa “zinthu zofunika kwambiri”?​—Afi 1:10