Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova

Muzithandiza Ophunzira Anu Kuti Akhale pa Ubwenzi ndi Yehova

Yehova amafuna kuti tizimutumikira chifukwa choti timamukonda. (Mt 22:37, 38) Kukonda Mulungu n’kumene kungathandize ophunzira Baibulo kuti asinthe komanso akhalebe olimba akamakumana ndi mayesero. (1Yo 5:3) Ndiponso kukonda Mulungu ndi komwe kumawathandiza kuti abatizidwe.

Muziwathandiza ophunzira anu kuti aziona kuti Mulungu amawakonda. Muziwafunsa mafunso monga: “Kodi zimenezi zikukuphunzitsani chiyani zokhudza Yehova?” kapena “Kodi zimenezi zikusonyeza bwanji kuti Yehova amakukondani?” Muziwathandiza kuti aziona mmene Yehova akuwathandizira paokha. (2Mb 16:9) Muziwafotokozera zitsanzo za mmene Yehova wakhala akuyankhira mapemphero anu, ndipo muziwalimbikitsa kuti aziona mmene akuyankhira mapemphero awo. Timasangalala kwambiri tikaona ophunzira Baibulo athu akukondedwa ndi Yehova, iwonso n’kumamukonda ndiponso kumayesetsa kuti akhale naye pa ubwenzi wolimba.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI AKHALE PA UBWENZI NDI YEHOVA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Jane anakumana ndi vuto liti?

  • Kodi Anita anathandiza bwanji Jane?

  • Kodi Jane anakwanitsa bwanji kuthana ndi vutolo?