Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa

Muzithandiza Ophunzira Baibulo Kuti Asiye Makhalidwe Oipa

Anthu okhawo amene ali ndi makhalidwe abwino, ndi amene angakhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. (1Pe 1:14-16) Ophunzira Baibulo akasiya makhalidwe oipa, zinthu zingamawayendere bwino m’banja, sangakumane ndi mavuto azachuma komanso angakhale ndi thanzi labwino.

Muziwafotokozera momveka bwino mfundo za makhalidwe abwino za Yehova, chifukwa chake mfundozo zilipo komanso kufunika kozitsatira. Muzithandiza ophunzira anu kuti asinthe mmene amaganizira, ndipo akatero, adzayamba kuchita zimene Yehova amasangalala nazo. (Aef 4:22-24) Muziwatsimikizira kuti mothandizidwa ndi Yehova, akhoza kusiya makhalidwe oipa. (Afi 4:13) Muziwaphunzitsa kuti azichonderera Yehova akaona kuti ayamba kulakalaka kuchita zinthu zoipa. Muziwaphunzitsa kuti azipewa zochitika zimene zingawachititse kuti ayesedwe. Muziwalimbikitsa kuti azichita zinthu zimene zingawathandize m’malo mochita zinthu zoipa. Mudzasangalala kwambiri mukadzaona ophunzira Baibulo anu akukwanitsa kusintha makhalidwe awo oipa mothandizidwa ndi Yehova.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZITHANDIZA AMENE MUKUPHUNZIRA NAWO BAIBULO KUTI ASIYE MAKHALIDWE OIPA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi akulu komanso Anita anasonyeza bwanji kuti ankakhulupirira Jane?

  • Kodi Anita anapitiriza bwanji kuthandiza Jane?

  • Kodi Jane anafufuza bwanji thandizo lochokera kwa Yehova?