MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Muziwerenga Baibulo Tsiku Lililonse Komanso Muzifunafuna Nzeru
Nzeru zochokera kwa Mulungu ndi zamtengo wapatali mofanana ndi chuma chobisika. (Miy 2:1-6) Nzeru zimatithandiza kuti tiziganiza bwino, tizisankha bwino zochita komanso zimatiteteza. Choncho “nzeru ndiyo chinthu chofunika kwambiri.” (Miy 4:5-7) Pamafunika khama kuti tifufuze chuma chauzimu chobisika cha m’Mawu a Mulungu. Tikhoza kuyamba ndi kuwerenga Mawu a Mulungu “usana ndi usiku,” kapena kuti tsiku lililonse. (Yos 1:8) Onani mfundo zimene zingatithandize kuti tiziwerenga komanso kusangalala ndi Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku.
ONERANI VIDIYO YAKUTI ACHINYAMATA AKUPHUNZIRA KUKONDA MAWU A MULUNGU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:
Kodi achinyamatawa anakumana ndi mavuto otani pamene ankafuna kuti aziwerenga Baibulo tsiku lililonse, nanga n’chiyani chimene chinawathandiza?
-
Melanie
-
Samuel
-
Celine
-
Raphaello
NDANDANDA YANGA YOWERENGERA BAIBULO: