MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mmene Tingagwiritsire Ntchito Mavidiyo Onena za Kuphunzira Baibulo
Tili ndi mavidiyo 4 onena za kuphunzira Baibulo omwe timagwiritsa ntchito tikakhala mu utumiki. Kodi iliyonse mwa mavidiyowa inakonzedwa ndi cholinga chotani?
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo?—Vidiyo Yathunthu inakonzedwa ndi cholinga choti izithandiza anthu kukhala ndi chidwi chokhudza Baibulo posatengera chipembedzo chawo. Imalimbikitsa anthu kuti azifufuza m’Baibulo mayankho a mafunso akuluakulu okhudza moyo ndipo imapereka chitsanzo cha mayankho ogwira mtima omwe amapezekamo. Imafotokoza mmene munthu angapemphere phunziro la Baibulo.
N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? (vidiyo yaifupi) ndi yofanana ndi vidiyo yathunthu koma ndi yaifupiko. Imathandiza kwambiri mu gawo limene anthu ake amakhala pa changu.
Vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? inakonzedwa ndi cholinga choti izikopa chidwi cha anthu chokhudza phunziro la Baibulo laulere komanso imayankha mafunso amene anthu amafunsa kawirikawiri okhudza phunziroli kuphatikizapo zimene angachite kuti apemphe phunziro la Baibulo.
Vidiyo yakuti Sangalalani Pophunzira Baibulo inakonzedwa kuti tizionetsa ophunzira Baibulo. Ngakhale kuti vidiyoyi inatchulidwa pa tsamba 2 la buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale, ikhoza kuonetsedwa mukamaphunzira kabuku. Vidiyoyi imafotokoza zimene zili m’bukuli komanso zimene wophunzira angayembekezere pa nthawi ya phunziro.
Ngakhale kuti vidiyo iliyonse inakonzedwa ndi cholinga chapadera, iliyonse ikhoza kuonetsedwa kapena kutumizidwa kwa munthu pamene zikufunika kutero. Ofalitsa akulimbikitsidwa kuti awadziwe bwino mavidiyowa komanso aziwagwiritsa ntchito moyenera akakhala mu utumiki.