March 20-26
2 MBIRI 1-4
Nyimbo Na. 41 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mfumu Solomo Inasankha Zinthu Mopanda Nzeru”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
2Mb 1:11, 12—Kodi nkhaniyi ikutiphunzitsa chiyani zokhudza mapemphero athu? (w05 12/1 19 ¶6)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) 2Mb 4:7-22 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Kuitanira Anthu ku Chikumbutso: (3 min.) Itanirani mnzanu wakuntchito, wakusukulu kapena wachibale wanu. (th phunziro 2)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Pangani ulendo wobwereza kwa munthu amene anasonyeza chidwi ndipo analandira kapepala komuitanira ku Chikumbutso. Mufotokozereni zokhudza phunziro la Baibulo la ulele, kenako mugawireni kabuku kakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. Yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji?, kenako kambiranani naye mfundo za muvidiyoyi. (th phunziro 17)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) lff phunziro 09 mfundo 5 (th phunziro 9)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Kodi Mwalikonzekera Tsiku Lofunika Kwambiri la Pachaka?: (15 min.) Nkhani komanso vidiyo. Ikambidwe ndi woyang’anira utumiki. Fotokozani mmene ntchito yoitanira anthu ku Chikumbutso ikuyendera. Funsani mafunso anthu amene akumana ndi zosangalatsa. Tchulani za ndandanda yowerengera Baibulo pa nyengo ya Chikumbutso yomwe ili pa tsamba 8 ndi 9, ndipo limbikitsani onse kuti akonzekeretse mitima yawo. (Eza 7:10) Kambiranani zimene tingachite kuti tidzalandire bwino alendo athu pa Tsiku la Chikumbutso. (Aro 15:7; mwb16.03 2) Onerani vidiyo yakuti, Mmene Mungapangire Mkate wa Chikumbutso.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff phunziro 41 mfundo 1-4
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 135 ndi Pemphero