Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

‘Mtima Wanga Udzakhala Pamenepa Nthawi Zonse’

‘Mtima Wanga Udzakhala Pamenepa Nthawi Zonse’

Yehova anasankha kachisi wake (2Mb 7:11, 12)

Yehova ananena kuti mtima wake udzakhalabe kumeneko nthawi zonse, zomwe zikusonyeza kuti adzapitiriza kuchita chidwi ndi zinthu zimene zikuchitika panyumba yodziwika ndi dzina lake (2Mb 7:16; w02 11/15 5 ¶1)

Ngati atasiya kutumikira Yehova “ndi mtima wawo wonse,” iye adzalola kuti kachisi awonongedwe (2Mb 6:14; 7:19-21; it-2 1077-1078)

Pamene ankapereka kachisi, anthu ankaganiza kuti mtima wawo udzakhala pa kachisipo nthawi zonse. Koma chomvetsa chisoni n’chakuti pang’ono ndi pang’ono anthuwa anasiya kutumikira Yehova ndi mtima wawo wonse.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndikusonyeza bwanji kuti ndimatumikira Yehova ndi mtima wonse?’