March 6-12
1 MBIRI 23-26
Nyimbo Na. 123 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Kulambira kwa Pakachisi Kunali kwa Dongosolo”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
1Mb 25:7, 8—Kodi malembawa akusonyeza bwanji kufunika koimba nyimbo zotamanda Yehova? (w22.03 22 ¶10)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) 1Mb 23:21-32 (th phunziro 5)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Vidiyo Yoitanira Anthu ku Chikumbutso: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyo ya chitsanzo cha Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso. Muziimitsa vidiyoyi nthawi iliyonse imene pali chizindikiro chosonyeza kuti muime n’kufunsa omvera mafunso omwe ali muvidiyoyi.
Kuitanira Anthu ku Chikumbutso: (3 min.) Yambani ndi chitsanzo cha zimene tinganene poitanira anthu ku Chikumbutso. Ngati mwininyumba wasonyeza chidwi yerekezerani kumuonetsa vidiyo yakuti Tizikumbukira Imfa ya Yesu, kenako kambiranani naye mfundo za muvidiyoyi. (th phunziro 11)
Nkhani: (5 min.) w11 6/1 14-15—Mutu: N’chifukwa Chiyani Akhristu Amachita Zinthu Mwadongosolo? (th phunziro 14)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
“Mmene Tingathandizire Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi”: (10 min.) Nkhani yokambirana komanso vidiyo.
Ntchito Yoitanira Anthu ku Chikumbutso Idzayamba Loweruka pa 11 March: (5 min.) Nkhani yokambirana. Onani mwachidule zimene zili pa kapepala koitanira anthu ku Chikumbutso. Fotokozani zimene mpingo wanu wakonza zokhudza kudzamvetsera nkhani yapadera ndi mwambo wa Chikumbutso komanso zomwe mudzachite kuti mudzathe kugawira timapepalati kwa anthu onse a m’gawo lanu.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff phunziro 39 ndi mawu akumapeto 3
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 127 ndi Pemphero