MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Mmene Tingathandizire Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi
Ngozi zam’chilengedwe zikuchitikachitika masiku ano. Ngozizi zikachitika, ntchito yothandiza anthu imafunika ichitike mwadongosolo komanso moyenera. Pachifukwa chimenechi, Bungwe Lolamulira linakonza kuti pa ofesi ya nthambi iliyonse pakhale Dipatimenti Yothandiza Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi.
Abale a mu dipatimentiyi akadziwa kuti pachitika ngozi, mwamsanga iwo amalumikizana ndi akulu a mu deralo kuti adziwe thandizo lomwe ofalitsa akufunikira. Ngati zinthu zawonongeka kwambiri moti ofalitsa sangakwanitse kukonza paokha, ofesi ya nthambi imapempha abale oyenerera kuti atsogolere ntchito yopereka thandizo. Abalewa angapemphe ofalitsa ongodzipereka kuti akathandize pa ntchitoyo kapena angapemphe abale ndi alongo kuti apereke zinthu zomwe zikufunikira. Nthawi zina akhoza kugula kudera lawo lomwelo zinthu zomwe zikufunikazo n’kukazipereka kwa amene akufunikira thandizowo.
Kuchita zinthu mwanjira imeneyi n’kothandiza kwambiri. Kumathandiza kuti anthu asamangogwira ntchito imodzimodziyo, kuti pasakhale chisokonezo komanso kuti pasawonongeke ndalama ndi zinthu zofunikira zomwe zikhoza kuchitika ngati aliyense atangoyamba kupereka thandizo payekha.
Abale omwe anasankhidwa ndi ofesi ya nthambi angaone kuchuluka kwa ndalama zomwe zikufunika komanso kuchuluka kwa anthu ongodzipereka oti akathandize pantchitoyo. Akhozanso kulankhula ndi akuluakulu a boma a m’deralo omwe nthawi zambiri amathandiza kuti ntchito yathu yopereka thandizo iyende bwino. Ndiye panokha musamatolere ndalama, kutumiza chithandizo kapena kupita kudera lomwe lakhudzidwa, pokhapokha ngati mwapemphedwa kutero.
Komabe, pakachitika ngozi yadzidzidzi timafuna kuthandiza. (Ahe 13:16) Timakonda abale ndi alongo athu. Ndiye tingatani? Chinthu chofunika kwambiri chomwe tingachite ndi kupempherera abale ndi alongo athu omwe akhudzidwa ndi ngozizo komanso amene akugwira ntchito yopereka thandizo. Tikhozanso kupereka ndalama ku ntchito ya padziko lonse. Motsogoleredwa ndi Bungwe Lolamulira, maofesi a nthambi ndi amene ali pa malo abwino kwambiri odziwa kumene ndalamazi zingakathandize. Ngati tikufuna kupita kukathandiza komwe kwachitika ngozi, tikhoza kulemba Fomu ya Wofuna Kutumikira Mongodzipereka m’Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga (DC-50).
ONERANI VIDIYO YAKUTI MADZI OSEFUKIRA OMWE ANAWONONGA KU BRAZIL, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:
Kodi chakusangalatsani n’chiyani chokhudza ntchito yopereka thandizo yomwe a Mboni za Yehova anagwira ku Brazil kutasefukira madzi mu 2020?