April 14-20
MIYAMBO 9
Nyimbo Na. 56 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Mukhale Anzeru, Osati Onyoza
(10 min.)
Munthu wonyoza amakana kulandira malangizo achikondi ndipo amakwiyira munthu amene akumupatsa malangizoyo (Miy 9:7, 8a; w22.02 9 ¶4)
Munthu wanzeru amayamikira malangizo komanso wopereka malangizoyo (Miy 9:8b, 9; w22.02 12 ¶12-14; w01 5/15 30 ¶1-2)
Munthu wanzeru adzapindula ndi nzeruzo, koma wonyoza adzavutika (Miy 9:12; w01 5/15 30 ¶5)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
Miy 9:17—Kodi “madzi akuba” n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani “amatsekemera”? (w06 9/15 17 ¶5)
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 9:1-18 (th phunziro 5)
4. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo anabwera ku Chikumbutso. (lmd phunziro 8 mfundo 3)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Munthuyo munamuthandizapo kupeza malo amene kukachitikire Chikumbutso kufupi ndi kwawo. (lmd phunziro 7 mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Munathandizapo wachibale wanu kupeza malo amene kukachitikire Chikumbutso kufupi ndi kwawo. (lmd phunziro 8 mfundo 4)
Nyimbo Na. 84
7. Kodi Mwayi wa Utumiki Umakuchititsani Kukhala Apadera?
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Onerani VIDIYO. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
Kodi mawu akuti “utumiki” amatanthauza chiyani?
Kodi anthu amene ali ndi maudindo mumpingo ayenera kumadziona bwanji?
N’chifukwa chiyani kutumikira ena n’kofunika kwambiri kuposa kulamulira ena?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 25 ¶5-7, bokosi patsamba 200