April 21-27
MIYAMBO 10
Nyimbo Na. 76 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Kodi N’chiyani Chimathandiza Munthu Kumasangalaladi pa Moyo?
(10 min.)
Munthu amene amakhaladi wosangalala ndi amene amagwira ntchito mwakhama pothandiza ena kudziwa za Yehova (Miy 10:4, 5; w01 7/15 25 ¶1-3)
Kukhala wolungama n’kofunika kwambiri kuposa chuma (Miy 10:15, 16; w01 9/15 24 ¶3-4)
Munthu amene amadalitsidwa ndi Yehova ndi amene amakhaladi wosangalala (Miy 10:22; it-1 340)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Miy 10:22—N’chifukwa chiyani atumiki a Mulungu amakumana ndi mavuto ambiri chonsecho madalitso a Yehova sawonjezerapo ululu? (w06 5/15 30 ¶18)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 10:1-19 (th phunziro 10)
4. Ulendo Woyamba
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Munthuyo wakuuzani kuti sakhulupirira kuti kuli Mulungu. (lmd phunziro 4 mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. M’pempheni kuti muziphunzira naye Baibulo. (lmd phunziro 4 mfundo 4)
6. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Musonyezeni mmene angapezere nkhani yomwe ingamusangalatse pa jw.org. (lmd phunziro 9 mfundo 4)
Nyimbo Na. 111
7. Kodi Ndi Madalitso Ati Amene Amalemeretsa Atumiki a Mulungu?
(7 min.) Nkhani yokambirana.
Madalitso amene Yehova amapereka kwa atumiki ake m’masiku otsiriza ovuta ano, amatithandiza kuti tizipirira komanso tizikhala osangalala. (Sl 4:3; Miy 10:22) Werengani malemba ali m’munsimu, kenako funsani omvera mmene dalitso lililonse limawathandizira kukhala osangalala.
Ena akwanitsa kuwonjezera utumiki wawo ndiponso kumasangalala kwambiri pa moyo wawo.
Onerani VIDIYO yakuti Achinyamata—Sankhani Njira Yomwe Ingakubweretsereni Mtendere. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
Kodi mwaphunzira chiyani kuchokera pa zimene zinachitikira Harley, Anjil ndi Carlee?
8. Lipoti la Dipatimenti Yoona za Mapulani Ndi Zomangamanga la 2025
(8 min.) Nkhani. Onerani VIDIYOYI.
9. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 25 ¶8-13, bokosi patsamba 201