April 7-13
MIYAMBO 8
Nyimbo Na. 89 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzimvetsera Nzeru Yomwe Ikulankhula Ngati Munthu
(10 min.)
Yesu, yemwe akutchulidwa kuti “nzeru” m’buku la Miyambo, anali “woyamba kulengedwa ndi Yehova” (Miy 8:1, 4, 22; cf 131 ¶7)
Yesu anakhala ndi nzeru kwambiri komanso anayamba kukonda kwambiri Atate wake chifukwa chokhala nthawi yaitali pambali pa Yehova n’kumagwira nawo ntchito yolenga (Miy 8:30, 31; cf 131-132 ¶8-9)
Tikamamvetsera nzeru za Yesu m’pamene zimatithandiza (Miy 8:32, 35; w09 4/15 31 ¶14)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 8:22-36 (th phunziro 10)
4. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Yankhani mafunso amene munthu yemwe akuganiza zodzapezeka pa Chikumbutso ali nawo okhudza zomwe zimachitika pamwambowu. (lmd phunziro 9 mfundo 3)
5. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. Landirani munthu amene wabwera ku Chikumbutso atapeza kapepala komuitanira ku mwambowu pakhomo pake, ndipo muyankhe mafunso amene angakhale nawo pambuyo pamwambowu. (lmd phunziro 3 mfundo 5)
6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira
(5 min.) Nkhani. ijwbq na. 160—Mutu: N’chifukwa Chiyani Baibulo Limati Yesu Ndi Mwana wa Mulungu? (th phunziro 1)
Nyimbo Na. 105
7. Zofunika Pampingo
(15 min.)
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 25 ¶1-4, bokosi patsamba 199