March 17-23
MIYAMBO 5
Nyimbo Na. 122 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzitalikirana Kwambiri ndi Chiwerewere
(10 min.)
Chiwerewere chimaoneka chosangalatsa (Miy 5:3; w00 7/15 29 ¶1)
Zotsatira za chiwerewere zimakhala zowawa (Miy 5:4, 5; w00 7/15 29 ¶2)
Muzitalikirana kwambiri ndi chiwerewere (Miy 5:8; w00 7/15 29 ¶5)
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Miy 5:9—Kodi chiwerewere chingachititse bwanji munthu kupereka ‘ulemu wake kwa anthu ena’? (w00 7/15 29 ¶7)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 5:1-23 (th phunziro 5)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Itanirani ku Chikumbutso munthu amene si wa Chikhristu, ndipo mugwiritse ntchito webusaiti yathu ya jw.org kuti mupeze malo akufupi ndi kwawo omwe kukachitikire mwambowu. (lmd phunziro 6 mfundo 4)
5. Ulendo Wobwereza
(4 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Pa ulendo wapita, munthuyo analandira kapepala komuitanira ku Chikumbutso ndipo anasonyeza chidwi. (lmd phunziro 9 mfundo 5)
6. Kuphunzitsa Anthu
(5 min.) lff phunziro 16 zomwe taphunzira, kubwereza komanso zolinga. Wophunzira akafunsa ngati Yesu anali wokwatira, musonyezeni mmene angafufuzire kuti apeze yankho. (lmd phunziro 11 mfundo 4)
Nyimbo Na. 121
7. Yesetsani Kukhalabe Oyera Pamene Muli Pachibwenzi
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Mawu akuti chibwenzi angatanthauze pamene “mwamuna ndi mkazi amacheza limodzi kwa nthawi yaitali mosonyeza kuti amakondana.” Zimenezi zingachitike kaya ndi pagulu kapena kwa awiri, moonetsera kapena mobisa, pamasom’pamaso kapena poimbirana foni ngakhalenso kulemberana mameseji. Timaona kuti kukhala pachibwenzi si nkhani yoti anthu akufuna kumangocheza basi koma akufuna kudziwana bwino n’cholinga choti pamapeto pake akwatirane. Kodi anthu amene ali pachibwenzi, kaya akhale achinyamata kapena achikulire, angatani kuti apewe kuchita chiwerewere pa nthawi imene ali pachibwenziyo?—Miy 22:3.
Onerani VIDIYO yakuti Kukonzekera Banja—Gawo 1: Kodi Ndafika Poti N’kukhala ndi Chibwenzi?—Kachigawo Kake. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
-
N’chifukwa chiyani munthu sayenera kuyamba chibwenzi mpaka pamene akuona kuti wakonzeka kulowa m’banja? (Miy 13:12; Lu 14:28-30)
-
Kodi n’chiyani chakusangalatsani mukaona mmene makolo athandizira mwana wawo muvidiyoyi?
Werengani Miyambo 28:26. Kenako funsani mafunso otsatirawa:
-
Kodi anthu amene ali pachibwenzi angachite zotani kuti akonzekereretu kupewa kukhala awiriwiri pamalo amene angawachititse kuti achite chiwerewere?
-
N’chifukwa chiyani ndi nzeru kuti anthu akayamba chibwenzi azikambirana zomwe akuyenera kuchita kapena zomwe sakuyenera kuchita posonyezana chikondi monga kugwirana manja kapena kukisana?
Werengani Aefeso 5:3, 4. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
Kodi anthu amene ali pachibwenzi akuyenera kukumbukira chiyani akamalankhulana pafoni kapena pa malo ochezera a pa intaneti?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 24 ¶1-6