March 3-9
MIYAMBO 3
Nyimbo Na. 8 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)
1. Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Yehova
(10 min.)
Musamadzidalire koma muzikhulupirira Yehova (Miy 3:5; ijwbv nkhani na. 14 ¶4-5)
Muzisonyeza kuti mumakhulupirira Yehova pofunafuna malangizo ake komanso kuwatsatira (Miy 3:6; ijwbv nkhani na. 14 ¶6-7)
Muzipewa kudzidalira kwambiri (Miy 3:7; be 76 ¶4)
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndimafunafuna malangizo a Yehova pa zonse zomwe ndimachita pa moyo wanga?’
2. Mfundo Zothandiza
(10 min.)
-
Miy 3:3—Kodi chikondi chokhulupirika komanso kukhulupirika tingazimange bwanji m’khosi mwathu ndiponso kuzilemba pamtima pathu? (w06 9/15 17 ¶7)
-
Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
3. Kuwerenga Baibulo
(4 min.) Miy 3:1-18 (th phunziro 12)
4. Ulendo Woyamba
(3 min.) KUNYUMBA NDI NYUMBA. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (lmd phunziro 1 mfundo 5)
5. Ulendo Woyamba
(4 min.) KULALIKIRA M’MALO OPEZEKA ANTHU AMBIRI. Mufotokozereni za webusaiti yathu ya jw.org ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za webusaitiyi. (lmd phunziro 3 mfundo 3)
6. Nkhani
(5 min.) w11 3/15 14 ¶7-10—Mutu: Muzisonyeza Kuti Mumadalira Mulungu Mukakumana ndi Anthu Opanda Chidwi mu Utumiki. (th phunziro 20)
Nyimbo Na. 124
7. Muzisonyeza Kuti Mumakhulupirira Gulu la Yehova
(15 min.) Nkhani yokambirana.
Zikhoza kukhala zosavuta kukhulupirira malangizo opezeka m’Mawu achoonadi ouziridwa, Baibulo. Koma zikhoza kukhala zovuta kukhulupirira malangizo ochokera kwa anthu opanda ungwiro omwe amatsogolera gulu la Yehova, makamaka ngati sitikumvetsa kapena kugwirizana ndi malangizowo.
Werengani Malaki 2:7. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
N’chifukwa chiyani sitiyenera kudabwa kuti Yehova amagwiritsa ntchito anthu opanda ungwiro kuti azitsogolera anthu ake?
Werengani Mateyu 24:45. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira malangizo ochokera ku gulu la Yehova?
Werengani Aheberi 13:17. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
N’chifukwa chiyani tiyenera kugwirizana ndi zosankha za abale amene Yehova amawakhulupirira kuti azitsogolera mu gulu lake?
Onerani VIDIYO yakuti Lipoti la Bungwe Lolamulira la Nambala 9 la 2021—Kachigawo Kake. Kenako funsani funso lotsatirali:
-
Kodi malangizo amene tinalandira pa nthawi ya COVID-19, anakuthandizani bwanji kuti muzikhulupirira kwambiri gulu la Yehova?
8. Phunziro la Baibulo la Mpingo
(30 min.) bt mutu 23 ¶9-15, bokosi patsamba 184, 186