May 30–June 5
MASALIMO 26-33
Nyimbo Na. 23 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (Osapitirira 3 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Tizidalira Yehova Kuti Tikhale Olimba Mtima”: (10 min.)
Sal. 27:1-3—Tikamakumbukira kuti Yehova ndiye kuwala kwathu timakhala olimba mtima (w12 7/15 22-23 ndime 3-6)
Sal. 27:4—Chikhulupiriro chathu chimalimba kwambiri tikamakonda kulambira koona (w12 7/15 24 ndime 7)
Sal. 27:10—Yehova ndi wokonzeka kuthandiza atumiki ake ngakhale anthu ena atawasiya (w12 7/15 24 ndime 9-10)
Kufufuza Mfundo Zothandiza: (8 min.)
Sal. 26:6—Mofanana ndi Davide, kodi tingazungulire bwanji guwa la nsembe la Yehova? (w06 5/15 19 ndime 10)
Sal. 32:8—Kodi timapindula bwanji Yehova akamatipatsa nzeru? (w09 6/1 5 ndime 3)
Kodi ndaphunzira zotani zokhudza Yehova pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?
Kodi ndi mfundo ziti zimene ndaphunzira mlungu uno zimene ndingazigwiritse ntchito mu utumiki?
Kuwerenga Baibulo: (Osapitirira 4 min.) Masalimo 32:1–33:8
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (Osapitirira 2 min.) kt—Werengani lemba pogwiritsa ntchito foni kapena chipangizo china chamakono.
Ulendo Wobwereza: (Osapitirira 4 min.) Chitani chitsanzo chosonyeza mmene tingapemphere munthu amene timam’patsa magazini mwezi uliwonse kuti tiziphunzira naye Baibulo. Muonetseni vidiyo yakuti Kodi Phunziro la Baibulo Limachitika Bwanji? kuchokera pa Laibulale ya JW.
Phunziro la Baibulo: (Osapitirira 6 min.) jl Phunziro 9—Sonyezani mwachidule wophunzirayo mmene angagwiritsire nchito Laibulale ya JW pokonzekera misonkhano.
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 130
Zofunika pampingo: (15 min.) Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo. Nkhani.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) cl mutu 31 ndime 1-12
Mfundo Zimene Taphunzira Komanso za Mlungu Wamawa (3 min.)
Nyimbo Na. 16 ndi Pemphero