Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzisonyeza Chikondi M’banja

Muzisonyeza Chikondi M’banja

Chikondi ndi guluu ndipo chimagwirizanitsa pamodzi anthu a m’banja. Popanda chikondi, banja lingavutike kuti likhale logwirizana. Kodi amuna, akazi komanso makolo angasonyeze bwanji chikondi m’banja?

Mwamuna wachikondi amaganizira zofuna za mkazi wake, maganizo ake komanso mmene akumvera. (Aef 5:28, 29) Iye amapezera banja lake zofunika pamoyo, komanso amathandiza anthu a m’banja lake kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo amachititsa Kulambira kwa Pabanja nthawi zonse. (1Ti 5:8) Mkazi wachikondi amagonjera mwamuna wake komanso ‘amamulemekeza kwambiri.’ (Aef 5:22, 33; 1Pe 3:1-6) Mwamuna ndi mkazi ayenera kukhala okonzeka kukhululukirana ndi mtima wonse. (Aef 4:32) Makolo achikondi amachita chidwi ndi mwana aliyense ndipo onse amawaphunzitsa kuti azikonda Yehova. (De 6:6, 7; Aef 6:4) Kodi ana anu akukumana ndi mavuto otani kusukulu? Kodi amatani anzawo akamawakakamiza kuchita zinazake? Anthu onse m’banja akamakondana kwambiri, aliyense amadzimva kukhala wotetezeka.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZISONYEZA CHIKONDI CHOSATHA M’BANJA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi mwamuna wachikondi amasamalira bwanji mkazi wake?

  • Kodi mkazi wachikondi amasonyeza bwanji kuti amalemekeza kwambiri mwamuna wake?

  • Kodi makolo achikondi amathandiza bwanji ana awo kuti azikonda Mawu a Mulungu?