Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzisankha Zinthu Mwanzeru pa Nkhani ya Mowa

Muzisankha Zinthu Mwanzeru pa Nkhani ya Mowa

Akhristu onse ayenera kuchita zinthu modziletsa pa nkhani ya mowa. (Miy 23:20, 29-35; 1Ak 6:9, 10) Ngati Mkhristu wasankha kumwa mowa, sayenera kumwa kwambiri. Akuyeneranso kupeweratu kudalira mowa kuti achite zinazake komanso sakuyenera kukhumudwitsa anthu ena. (1Ak 10:23, 24; 1Ti 5:23) Sitikuyenera kukakamiza aliyense kuti amwe mowa, makamaka ana.

ONERANI VIDIYO YAMAKATUNI YAKUTI GANIZIRANI ZIMENE ZINGACHITIKE NGATI MUTAMWA MOWA, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani Akhristu onse ayenera kutsatira malamulo a m’dera lawo pa nkhani yomwa mowa?​—Aro 13:1-4

  • N’chifukwa chiyani sitiyenera kulola anthu ena kutikakamiza kuti timwe mowa?​—Aro 6:16

  • Kodi tingapewe bwanji mavuto omwe angabwere chifukwa cha mowa?