Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI | ZIMENE MUNGACHITE KUTI MUZISANGALALA KWAMBIRI MU UTUMIKI

Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse

Muziphunzitsa Ndi Mtima Wonse

Kuphunzitsa ndi mtima wonse kumachititsa kuti anthu amene tikuwaphunzitsa azimvetsera mwatcheru. Kumasonyezanso kuti timaona kuti uthenga wathu ndi wofunika. Tonsefe tingathe kumaphunzitsa ndi mtima wonse, posatengera komwe tinakulira kapena mmene tilili. (Aro 12:11) Tingachite bwanji zimenezi?

Choyamba, muziganizira kufunika kwa uthenga wanu. Muli ndi mwayi wolengeza “uthenga wabwino wa zinthu zabwino.” (Aro 10:15) Chachiwiri, muziganizira mmene uthenga wabwino ungathandizire omvera anu. Iwo akufunika kumva uthenga wanu. (Aro 10:13, 14) Chomaliza, muzisonyeza kuti nkhaniyo yakufikani pamtima ndipo manja ndi nkhope yanu zizisonyeza mmene mukumvera mumtima.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIWONJEZERA LUSO LANU KUTI MUZISANGALALA NDI NTCHITO YOPHUNZITSA​—MUZIPHUNZITSA NDI MTIMA WONSE, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi n’chiyani chinachititsa Anita kuti asiye kuphunzitsa Janendi mtima wonse?

  • Kodi n’chiyani chinathandiza Anita kuti ayambirenso kuphunzitsa Jane ndi mtima wonse?

  • Kuphunzitsa ndi mtima wonse kumathandiza anthu

    N’chifukwa chiyani tiyenera kumaganizira kwambiri za makhalidwe abwino a omvera athu?

  • Kodi kuphunzitsa ndi mtima wonse kungathandize bwanji amene timawaphunzitsa Baibulo komanso anthu ena?