CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
Muzikwaniritsa Zimene Mwalonjeza
Aisiraeli ankalonjeza zinthu mwakufuna kwawo koma ankafunika kukwaniritsa zimene alonjezazo (Nu 30:2; it-2 1162)
Malonjezo ena ankafuna kuti wolonjezayo azipewa zinthu zina ngakhale kuti zinthuzo sizolakwika (Nu 30:3, 4; it-2 1162)
Yehova masiku ano amachita zinthu ndi mtumiki wake aliyense payekha (Nu 30:6-9; w04 8/1 27 ¶3)
Malonjezo awiri ofunika kwambiri amene Mkhristu angapange masiku ano ndi lonjezo lokhudza kudzipereka kwa Mulungu komanso la ukwati.
DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndikuchita zinthu zonse zomwe ndinalonjeza?’