Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

Kupatsidwa Chilango Kumasonyeza Kuti Yehova Amatikonda

Mawu akuti chilango kwenikweni amatanthauza kupereka malangizo ndiponso kuphunzitsa munthu. Koma amaphatikizaponso kuthandiza munthu amene walakwitsa zinazake. Yehova amatipatsa chilango n’cholinga choti tizimulambira m’njira imene iye amafuna. (Aro 12:1; Ahe 12:10, 11) Nthawi zina chilango chimakhala chopweteka, koma chimathandiza munthu kukhala wolungama komanso kupeza madalitso. (Miy 10:7) Kodi amene akupereka komanso kulandira chilango ayenera kukumbukira zinthu ziti?

Wopereka. Akulu, makolo komanso anthu ena amayesetsa kupereka chilango mokoma mtima komanso mwachikondi ngati mmene Yehova amachitira. (Yer 46:28) Ngakhale chilango chitakhala champhamvu, chiyenera kuperekedwa mogwirizana ndi mmene zinthu zilili komanso mwachikondi.​—Tit 1:13.

Wolandira. Mulimonse mmene malangizo angaperekedwere, sitiyenera kuwakana koma tiyenera kuwagwiritsa ntchito nthawi yomweyo. (Miy 3:11, 12) Monga anthu opanda ungwiro, tonsefe timafunika malangizo omwe amabwera m’njira zosiyanasiyana. Tikhoza kulandira malangizo tikamawerenga Baibulo kapena pamisonkhano ya mpingo. Koma nthawi zina, ena amafunika kupatsidwa malangizo ndi komiti yoweruza mlandu. Tikamamvera malangizo komanso kuwagwiritsa ntchito tidzakhala ndi moyo wabwino panopa, komanso mpaka kalekale.​—Miy 10:17.

ONERANI VIDIYO YAKUTI “YEHOVA AMALANGA ALIYENSE AMENE IYE AMAMUKONDA,” NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi moyo wa Canon unali bwanji poyamba, nanga unasintha motani?

  • Kodi Yehova anam’patsa bwanji malangizo mwachikondi?

  • Muzikonda chilango chochokera kwa Yehova

    Kodi zimene zinachitikira Canon zikutiphunzitsa chiyani?