May 31–June 6
DEUTERONOMO 1–2
Nyimbo Na. 125 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Mukuweruzira Mulungu”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
De 1:19; 2:7—Kodi Yehova anasamalira bwanji anthu ake pa zaka 40 zimene ankayenda ‘m’chipululu chachikulu ndi chochititsa mantha’? (w13 9/15 9 ¶9)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) De 1:1-18 (th phunziro 10)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito chitsanzo cha ulendo woyamba. Sonyezani mmene mungayankhire munthu amene wanena zinthu zina zomwe anthu amakonda kunena ngati sakufuna kuti tikambirane nawo. (th phunziro 16)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Yambani ndi chitsanzo cha ulendo wobwereza. M’patseni kapepala koitanira anthu kumisonkhano yathu, ndipo kenako yerekezani kumuonetsa vidiyo yakuti Kodi pa Nyumba ya Ufumu Pamachitika Zotani? (th phunziro 11)
Nkhani: (5 min.) w13 8/15 11 ¶7—Mutu: Muzipewa Kulankhula Kapena Kumvetsera Nkhani Zoipa. (th phunziro 13)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Nyimbo Na. 30
“Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa ‘Masiku Otsiriza’”: (15 min.) Nkhani yokambirana yokambidwa ndi mkulu. Onerani vidiyo yakuti Zimene Tingachite Pokonzekera Masoka Achilengedwe. Tchulaninso zilengezo zochokera ku ofesi ya nthambi kapena ku bungwe la akulu ngati zilipo.
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) jy mutu 136
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 103 ndi Pemphero