Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa “Masiku Otsiriza”

Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa “Masiku Otsiriza”

Pamene tili kumapeto kwa “masiku otsiriza” ano, mavuto amene tikukumana nawo aziwonjezereka. (2Ti 3:1; nwtsty mfundo yothandiza pophunzira Mt 24:8) Kukachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, nthawi zambiri anthu a Yehova amalandira malangizo mwamsanga omwe akhoza kupulumutsa moyo wawo. Kuti tidzapulumuke kukadzachitika ngozi zadzidzidzi m’tsogolo, tikufunika kukonzekera panopa, mwakuthupi komanso mwauzimu.​—Lu 16:10.

  • Konzekerani mwauzimu: Khalani ndi dongosolo labwino lochitira zinthu zauzimu. Phunzirani njira zosiyanasiyana zolalikirira. Musade nkhawa ngati kwa kanthawi simukutha kuchitanso zinthu limodzi ndi mpingo wanu. (Yes 30:15) Muzikumbukira kuti Yehova komanso Yesu ali nanu nthawi zonse.​—od 176 ¶15-17

  • Konzekerani mwakuthupi: Kuwonjezera pa kukhala ndi chikwama chomwe muli zinthu zofunika zomwe mungatenge ngati patachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, banja lililonse liyenera kusunga chakudya chokwanira, madzi, mankhwala, komanso zinthu zina zomwe lingagwiritse ntchito ngati patafunika kuti lisachoke panyumba kwa nthawi yayitali ndithu.​—Miy 22:3; g17.5 4, 6

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGACHITE POKONZEKERA MASOKA ACHILENGEDWE, NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tingakonzekere bwanji mwauzimu masoka asanachitike?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera . . .

    • kumalankhula ndi akulu nthawi zonse?

    • kukhala ndi zinthu zomwe tingazigwiritse ntchito pakachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi?

    • kukambirana mitundu ya masoka omwe angachitike komanso zimene tingachite masokawo akachitika?

  • Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tingachite pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi tsoka linalake?

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi mliri wa COVID-19 wandiphunzitsa chiyani pa nkhani yokhala wokonzeka?’