Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Musalole Kuti Zilakolako Zoipa Zizikulamulirani

Musalole Kuti Zilakolako Zoipa Zizikulamulirani

Davide analola kuti zilakolako zoipa zikhazikike mumtima mwake (2Sa 11:2-4; w21.06 17 ¶10)

Davide anagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwika kuti abise tchimo lomwe anachita (2Sa 11:5, 14, 15; w19.09 17 ¶15)

Davide anakumana ndi mavuto aakulu chifukwa cha tchimo lomwe anachita (2Sa 12:9-12; w18.06 17 ¶7)

Kuti tipewe kuyang’ana kapena kuganizira zinthu zolakwika, tiyenera kukhala odziletsa. (Aga 5:16, 22, 23) Yehova akhoza kutithandiza kuti zilakolako zoipa zisakhazikike mumtima mwathu.

DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi ndiyenera kudziletsa kwambiri ndikamaganizira zinthu ziti?