Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzidziletsa

Muzidziletsa

Monga anthu opanda ungwiro, nthawi zina zimativuta kuti tizilamulira zomwe timalakalaka. Titamangochita zilizonse zomwe tikufuna, Yehova sangamasangalale nafe. Mwachitsanzo, anthu ena amakonda kwambiri zakudya, zovala komanso malo okhala kuposa mmene amakondera Mulungu. Enanso amakhutiritsa zilakolako zawo zakugonana m’njira imene imaphwanya mfundo za Mulungu. (Aro 1:26, 27) Pamene enanso amangotengera zochita za anzawo n’cholinga choti aziwakonda komanso asaoneke otsalira.​—Eks 23:2.

Kodi tingatani kuti tizilamulira zimene timalakalaka? Tikuyenera kuchita zonse zimene tingathe kuti tiziona kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ndi umene uli wofunika kwambiri. (Mt 4:4) Tiyeneranso kupempha Yehova kuti atithandize kukhala odziletsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa amadziwa zimene zili zabwino kwa ife komanso mmene angakhutiritsire zolakalaka zathu zoyenera.​—Sl 145:16.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUSAWONONGE MOYO WANU CHIFUKWA CHA KUSUTA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani anthu ena amasuta?

  • Kodi kusuta kungakukhudzeni bwanji?

  • N’chifukwa chiyani kusuta komanso kuvepa n’koipa?​—2Ak 7:1

  • Mukhoza kuthana ndi chibaba

    Kodi mungakane bwanji ngati wina atakuuzani kuti musute? Nanga mungathetse bwanji chizolowezi chosuta?