Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzigwiritsa Ntchito Buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale Polimbitsa Chikhulupiriro Chanu mwa Yehova Ndi Yesu

Muzigwiritsa Ntchito Buku Lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale Polimbitsa Chikhulupiriro Chanu mwa Yehova Ndi Yesu

Ophunzira Baibulo ayenera kukhala ndi chikhulupiriro cholimba kuti azisangalatsa Mulungu. (Ahe 11:6) Tingawathandize kuchita zimenezi tikamagwiritsa ntchito buku lakuti Mungakhale Ndi Moyo Mpaka Kalekale. M’bukuli muli malemba ofunika, limafotokoza mfundo momveka bwino, muli mafunso othandiza kuganiza, mavidiyo okopa chidwi komanso zithunzi zokongola. Tikamathandiza ophunzira anthu kukhala ndi makhalidwe abwino komanso kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu, timakhala tikumanga ndi zomangira zosagwira moto.​—1Ak 3:12-15.

Anthu ena amaona kuti n’zovuta kukhala pa ubwenzi ndi Mulungu yemwe sangamuone. Choncho tiyenera kuwathandiza kuti amudziwe bwino Yehova komanso kuti azimukhulupirira.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZILIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHANU MWA YEHOVA POGWIRITSA NTCHITO BUKU LAKUTI “MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti mlongoyu anakonzekera bwino phunziroli?

  • Kodi anagwiritsa ntchito bwanji mafunso owonjezera pofuna kuthandiza wophunzira wake kuti afotokoze maganizo ake pa lemba la Yesaya 41:10, 13?

  • Kodi vidiyo imene anaonera komanso mavesi amene anawerenga anamuthandiza bwanji wophunzirayo?

Anthu ambiri samvetsa zokhudza dipo kapenanso samaliona kuti ndi mphatso imene Mulungu anawapatsa. (Aga 2:20) Choncho tiziwathandiza kuti azikhulupirira kwambiri nsembe ya dipo ya Yesu.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZILIMBITSA CHIKHULUPIRIRO CHANU MWA YESU POGWIRITSA NTCHITO BUKU LAKUTI “MUNGAKHALE NDI MOYO MPAKA KALEKALE,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tikudziwa bwanji kuti m’baleyu anakonzekera bwino phunziroli?

  • Kodi anagwiritsa ntchito bwanji gawo lakuti “Onani Zinanso” kuti athandize wophunzirayo?

  • N’chifukwa chiyani wophunzira Baibulo ayenera kumapemphera payekha?