Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Chikondi . . . Sichidzikuza”

“Chikondi . . . Sichidzikuza”

Chikondi chimatithandiza kuti tizisonyeza kuti ndife odzichepetsa. (1Ak 13:4) Tikamakonda abale athu, sitimadziona kukhala ofunika kwambiri kuposa iwowo. Timaona zabwino mwa anthu ena ndipo timagwiritsa ntchito maluso athu powathandiza. (Afi 2:3, 4) Tikamakonda kwambiri abale athu, ndi pamene Yehova angamatigwiritse ntchito pochita chifuniro chake.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIKUMBUKIRA ZIMENE CHIKONDI CHIMACHITA KOMANSO ZIMENE SICHICHITA​—SICHIDZIKUZA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Abisalomu anali ndi mphatso ziti?

  • Kodi anagwiritsa ntchito bwanji molakwika mphatso zakezi?

  • Kodi tingatani kuti tipewe kudzikuza?​—Aga 5:26