Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Chikondi . . . Chimayembekezera Zinthu Zonse”

“Chikondi . . . Chimayembekezera Zinthu Zonse”

Chikondi chimatithandiza kuti tizifunira zabwino abale athu. (1Ak 13:4, 7) Mwachitsanzo, ngati m’bale kapena mlongo wachimwa n’kupatsidwa uphungu timayembekezera kuti autsatira ndipo asintha. Timaleza mtima ndi anthu omwe ali ndi chikhulupiriro chofooka ndipo timayesetsa kuwathandiza. (Aro 15:1) Ngati wina wasiya kusonkhana ndi mpingo, sitimataya mtima koma timayembekezera kuti tsiku lina adzabwerera.​—Lu 15:17, 18.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIKUMBUKIRA ZIMENE CHIKONDI CHIMACHITA KOMANSO ZIMENE SICHICHITA​—CHIMAYEMBEKEZERA ZINTHU ZONSE, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Abineri anasintha bwanji?

  • Kodi Davide komanso Yowabu anachita bwanji zinthu ndi pempho la Abineri?

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kuyembekezera zabwino kuchokera kwa abale athu?