Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

“Chikondi . . . Sichikondwera ndi Zosalungama”

“Chikondi . . . Sichikondwera ndi Zosalungama”

Zinthu zonse zimene Akhristu oona amachita, zimatsogoleredwa ndi chikondi. Chikondi “Sichikondwera ndi zosalungama.” (1Ak 13:4, 6) Choncho tiyenera kupeweratu zosangalatsa zimene zimalimbikitsa zachiwerewere komanso zachiwawa. Ndiponso sitimasangalala anthu ena akamakumana ndi zinthu zoipa, ngakhale amene anatilakwira.​—Miy 17:5.

ONERANI VIDIYO YAKUTI MUZIKUMBUKIRA ZIMENE CHIKONDI CHIMACHITA KOMANSO ZIMENE SICHICHITA​—SICHIKONDWERA NDI ZOSALUNGAMA, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Davide anatani atauzidwa kuti Yonatani ndi Sauli aphedwa?

  • Kodi ndi nyimbo yoimba polira iti imene Davide anapekera Sauli ndi Yonatani?

  • N’chifukwa chiyani Davide sanasangalale atamva kuti Sauli wamwalira?