Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mwakonzeka Kukumana Ndi Zachiwawa?

Kodi Mwakonzeka Kukumana Ndi Zachiwawa?

Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, zachiwawa, uchigawenga komanso nkhondo ziziwonjezerekabe. (Chv 6:4) Kodi tingakonzekere bwanji mavutowa panopa?

  • Muzikonzekera mwauzimu: Fufuzani mfundo komanso nkhani za m’Baibulo zomwe zingakuthandizeni kuti muzikhulupirira kwambiri Yehova ndi gulu lake komanso kuti musakhale mbali ya dziko. (Miy 12:5; jr 125-126 ¶23-24) Ino ndiyo nthawi yoti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi abale ndi alongo mumpingo.​—1Pe 4:7, 8

  • Muzikonzekera mwakuthupi: Muzidziwiratu malo amene mungakakhaleko motetezeka komanso zinthu zofunika zokwanira ndipo muzikonzekereratu mmene mungachokere panyumba. Muzionanso zimene munasunga mu chikwama chanu chomwe mumaikamo zinthu zofunika zomwe mungatenge ngati patachitika ngozi zadzidzidzi, kuphatikizapo ndalama komanso zinthu zodzitetezera ku matenda monga magulovesi ndi masiki. Muzidziwa mmene mungalumukizirane ndi akulu ndipo muzionetsetsa kuti ali ndi nambala yanu ya foni.​—Yes 32:2; g17.5 3-7

Kukamachitika zipolowe, muzionetsetsa kuti mukupitirizabe kuchita zinthu zomwe mumachita polambira Yehova monga kupemphera, kuphunzira panokha komanso kupezeka pamisonkhano. (Afi 1:10) Musamayendeyende kupatulapo ngati pakufunika kutero. (Mt 10:16) Muzigawana zakudya komanso zinthu zina.​—Aro 12:13.

ONERANI VIDIYO YAKUTI KODI MWAKONZEKA KUKUMANA NDI NGOZI ZOGWA MWADZIDZIDZI?, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi Yehova angatithandize bwanji pa nthawi imene kwachitika ngozi zadzidzidzi?

  • Kodi tingakonzekere bwanji?

  • Kodi tingathandize bwanji anthu ena amene akhudzidwa ndi ngozizi?