Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Davide akuganizira mozama za pangano limene Yehova anapangana naye

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yehova Anachita Pangano ndi Davide

Yehova Anachita Pangano ndi Davide

Yehova analonjeza Davide kuti adzakhazikitsa ufumu m’banja lake (2Sa 7:11, 12; w10 4/1 20 ¶3; onani chithunzi chapachikuto)

Mbali zina za pangano limene Yehova anachita ndi Davide zinakwaniritsidwa pa Mesiya (2Sa 7:13, 14; Ahe 1:5; w10 4/1 20 ¶4)

Zinthu zabwino zimene zinabwera chifukwa cha ulamuliro wa Mesiya zidzakhalapo mpaka kalekale (2Sa 7:15, 16; Ahe 1:8; w14 10/15 10 ¶14)

Dzuwa ndi mwezi zimatikumbutsa kuti ulamuliro wa Mesiya udzakhalapo mpaka kalekale. (Sl 89:35-37) Mukamaona zinthu zimenezi muziganizira madalitso amene Yehova anakulonjezani inuyo komanso anthu a m’banja lanu kudzera mu Ufumu wake.