Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Dzitetezeni kwa Anthu Ampatuko

Dzitetezeni kwa Anthu Ampatuko

Satana ndi anthu ake nthawi zambiri amasakaniza choonadi ndi bodza pofuna kufooketsa chikhulupiriro chathu. (2Ak 11:3) Mwachitsanzo, Asuri sanafotokoze mmene nkhani yonse inalili ndipo ananena zinthu zabodza pofuna kufooketsa anthu a Yehova. (2Mb 32:10-15) Ampatuko amachitanso zimenezi masiku ano. Kodi tizitani ndi zimene ampatuko amaphunzitsa? Tiziwaona kuti ndi poizoni. Tisamawerenge nkhani zawo, tisamawayankhe komanso tisamaonere mavidiyo awo. Tizizindikira mwamsanga komanso kukana zinthu zomwe zakonzedwa n’cholinga chakuti zitichititse kukayikira Yehova komanso gulu lake.​—Yuda 3, 4.

ONERANI MBALI INA YA VIDIYO YAKUTI MENYA MWAMPHAMVU NKHONDO YACHIKHULUPIRIRO,” KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala osamala tikamagwiritsa ntchito intaneti?

  • Kodi tingatsatire bwanji malangizo opezeka pa Aroma 16:17?