Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mukugwiritsa Ntchito Mokwanira Baibulo Longomvetsera?

Kodi Mukugwiritsa Ntchito Mokwanira Baibulo Longomvetsera?

Kodi Baibulo longomvetsera ndi chiyani? Ndi Baibulo la Dziko Latsopano lokonzedwanso lochita kujambula. Baibuloli likutulutsidwa mwapang’onopang’ono m’zilankhulo zambiri. Chosangalatsa kwambiri ndi Baibuloli n’chakuti limamveka ndi mawu osiyanasiyana a anthu opezeka m’Baibulo omwe analankhula. Mawuwa amawerengedwa ndi mzimu wa nkhaniyo komanso amawatsindika moyenera kuti uthenga wa m’Baibulo umveke molondola.

Kodi Baibulo longomvetserali likuthandiza bwanji anthu? Ambiri amene amamvetsera Baibuloli amalikonda chifukwa limawathandiza kuona kuti mawu a Mulungu ndi amoyo. Amaona kuti akamamvetsera mawu a anthu osiyanasiyana, zimawathandiza kuona m’maganizo mwawo zimene zinkachitika komanso amamvetsa bwino zimene zinalembedwa m’Baibulo. (Miy 4:5) Amaonanso kuti kumvetsera Baibuloli, kumawakhazika mtima pansi akakhala ndi nkhawa.​—Sl 94:19.

Kumva mawu a Mulungu akuwerengedwa mokweza kumakhala ndi mphamvu kwambiri. (2Mb 34:19-21) Ngati Baibulo longomvetsera lilipo lathunthu kapena mbali yake chabe m’chilankhulo chimene mumamva, mukhoza kukonza zoti muzilimvetsera nthawi zonse mukamachita zinthu zokhudza kulambira.

ONERANI MBALI INA YA VIDIYO YAKUTI ZIMENE ZINACHITIKA POJAMBULA BAIBULO LONGOMVETSERA, KENAKO YANKHANI FUNSO LOTSATIRALI:

N’chiyani chakuchititsani chidwi mukaona zimene zinachitika pojambula Baibulo longomvetsera?