Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Muzidziona Mmene Yehova Amakuonerani

Muzidziona Mmene Yehova Amakuonerani

“Yehova amasangalala ndi anthu ake.” (Sl 149:4) Ngakhale kuti siife angwiro, iye amaona makhalidwe athu abwino komanso zomwe tingakwanitse kuchita. Komabe, nthawi zina zikhoza kutivuta kumadziona moyenera. Tikhoza kumamva ngati ndife osafunika chifukwa cha zimene ena amatichitira. Kapena, titamangoganizira zimene tinalakwitsa m’mbuyomu, tikhoza kumakayikira ngati Yehova angatikondedi. Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize tikamamva chonchi?

Tizikumbukira kuti Yehova amaona zambiri kuposa zimene anthu amaona. (1Sa 16:7) Zimenezi zikutanthauza kuti iye amaona zambiri mwa ife kuposa mmene timadzionera. N’zosangalatsa kuti Baibulo limatithandiza kumvetsa mmene Yehova amationera. Tingamvetse zimenezi tikamawerenga nkhani za m’Baibulo zomwe zimasonyeza mmene Yehova amakondera anthu amene amamulambira.

ONERANI VIDIYO YAKUTI TSIMIKIZIRANI MTIMA WANU KUTI YEHOVA SAKUKUIMBANI MLANDU, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi fanizo la munthu wothamanga komanso bambo ake likutiphunzitsa chiyani zokhudza mmene Yehova amationera?

  • Ngati munthu amene anachita tchimo wachita zonse zofunika kuti akonzenso ubwenzi wake ndi Yehova, kodi angatsimikizire bwanji mtima wake kuti Yehova sakumuimba mlandu?​—1Yo 3:19, 20

  • Kodi kuwerenga komanso kuganizira mozama nkhani ya Davide ndi Yehosafati kunathandiza bwanji m’baleyu?