May 22-28
2 MBIRI 25-27
Nyimbo Na. 80 ndi Pemphero
Mawu Oyamba (1 min.)
CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU
“Yehova Akhoza Kukupatsani Zambiri Kuposa Pamenepa”: (10 min.)
Mfundo Zothandiza: (10 min.)
2Mb 26:4, 5—Kodi chitsanzo cha Uziya chikutiphunzitsa chiyani zokhudza kufunika kokhala ndi munthu wolimba mwauzimu woti azitilangiza? (w07 12/15 10 ¶1-2)
Pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno, kodi mwapeza mfundo ziti zokhudza Yehova, utumiki kapena zinthu zina?
Kuwerenga Baibulo: (4 min.) 2Mb 25:1-13 (th phunziro 12)
KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI
Ulendo Woyamba: (3 min.) Gwiritsani ntchito nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo woyamba. Mufotokozereni kuti timaphunzira Baibulo ndi anthu ndipo m’patseni khadi lodziwitsa anthu za phunziro la Baibulo. (th phunziro 2)
Ulendo Wobwereza: (4 min.) Gwiritsani ntchito nkhani imene ili mu chitsanzo cha ulendo wobwereza. Mufotokozereni za webusaiti yathu ya jw.org, ndipo mugawireni khadi lodziwitsa anthu za webusaitiyi. (th phunziro 15)
Phunziro la Baibulo: (5 min.) lff phunziro 10 mawu oyamba komanso mfundo 1-3 (th phunziro 3)
MOYO WATHU WACHIKHRISTU
Moyo Wosatha ndi Wabwino Kwambiri Kuposa Zinthu Zimene Tingasiye (Mko 10:29, 30): (15 min.) Nkhani yokambirana. Onerani vidiyoyi. Kenako funsani mafunso otsatirawa: Kodi lonjezo la Yesu lopezeka pa Maliko 10:29, 30, likutilimbikitsa kuchita chiyani? Kodi Yesu anachita chiyani pamene abale ake sanamukhulupirire poyamba? Kodi tiyenera kumakumbukira chiyani zokhudza achibale athu omwe si a Mboni?
Phunziro la Baibulo la Mpingo: (30 min.) lff phunziro 46
Mawu Omaliza (3 min.)
Nyimbo Na. 51 ndi Pemphero