Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

“Yehova Akhoza Kukupatsani Zambiri Kuposa Pamenepa”

“Yehova Akhoza Kukupatsani Zambiri Kuposa Pamenepa”

Amaziya analemba ganyu asilikali kuti amenyane ndi adani a Mulungu (2Mb 25:5, 6)

Munthu wa Mulungu analangiza Amaziya kuti asagwiritse ntchito asilikaliwo (2Mb 25:7, 8; it-1 1266 ¶6)

Yehova akanabwezera Amaziya zinthu zambiri zoposa ndalama zomwe anawononga (2Mb 25:9, 10)

DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndingasiye zinthu ziti kuti ndizichita zambiri potumikira Yehova? Kodi ndi madalitso ati amene ndingapeze ngati nditachita zimenezi?’​—Mki 3:10; w21.08 30 ¶16.