Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Yehova ndi “Tate wa Ana Amasiye”

Yehova ndi “Tate wa Ana Amasiye”

Chaka chilichonse, achinyamata ambiri amasankha kukhala mabwenzi a Yehova. (Sl 110:3) Yehova amakukondani kwambiri. Iye amadziwa bwino mavuto amene aliyense payekha akukumana nawo ndipo analonjeza kuti adzakuthandizani kuti muzikwanitsa kumutumikira. Ngati mukuleredwa m’banja la kholo limodzi, muzikumbukira kuti Yehova ndi “tate wa ana amasiye.” (Sl 68:5) Yehova angakuthandizeni kuti zinthu zizikuyenderani bwino posatengera zimene mukukumana nazo kunyumba kwanu.​—1Pe 5:10.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ANTHU OMWE APAMBANA PA NKHONDO YACHIKHULUPIRIRO​—AMENE AKULEREDWA NDI KHOLO LIMODZI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • Kodi tikuphunzira chiyani pa zitsanzo za Tammy, Charles ndi Jimmy

  • Kodi ndi lonjezo liti lopezeka pa Salimo 27:10, lomwe lingalimbikitse achinyamata amene akuleredwa ndi kholo limodzi?