Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

June 3-9

MASALIMO 45-47

June 3-9

Nyimbo Na. 27 ndi Pemphero | Mawu Oyamba (1 min.)

CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU

Yesu ali ndi mkwatibwi wake omwe ndi a 144,000

1. Nyimbo ya Ukwati wa Mfumu

(10 min.)

Salimo la nambala 45 limafotokoza za ukwati wa Mfumu yomwenso ndi Mesiya (Sl 45:1, 13, 14; w14 2/15 9-10 ¶8-9)

Ukwati wa Mfumuwu udzachitika pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo (Sl 45:3, 4; w22.05 17 ¶10-12)

Anthu onse adzalandira madalitso chifukwa cha ukwatiwu (Sl 46:8-11; it-2 1169)


DZIFUNSENI KUTI, ‘Kodi mtima wanga “umasangalala” kulengeza uthenga wabwino wonena za Mfumu yathu, Yesu Khristu?’​—Sl 45:1.

2. Mfundo Zothandiza

(10 min.)

  • Sl 45:16​—Kodi vesili likutiphunzitsa chiyani zokhudza mmene moyo udzakhalire m’Paradaiso? (w17.04 11 ¶9)

  • Kodi ndi mfundo ziti zimene mwapeza pa kuwerenga Baibulo kwa mlungu uno?

3. Kuwerenga Baibulo

KUPHUNZITSA MWALUSO MU UTUMIKI

4. Ulendo Woyamba

(3 min.) KULALIKIRA MWAMWAYI. (lmd phunziro 1 mfundo 3)

5. Nkhani

(5 min.) ijwbv 26​—Mutu: Kodi lemba la Salimo 46:10 limatanthauza chiyani? (th phunziro 18)

6. Kufotokoza Zimene Mumakhulupirira

(4 min.) Chitsanzo. g 12/10 22-23​—Mutu: Kodi Nkhani ya Maukwati a Amuna Kapena Akazi Okhaokha Mumaiona Bwanji? (lmd phunziro 6 mfundo 5)

MOYO WATHU WA CHIKHRISTU

Nyimbo Na. 131

7. Pitirizani Kusonyezana Chikondi M’banja Lanu

(10 min.) Nkhani yokambirana.

Ukwati umakhala wosangalatsa kwambiri. (Sl 45:13-15) Nthawi zambiri, tsiku la ukwati limakhala lamtengo wapatali kwambiri kwa amene akwatiranawo. Koma kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti apitirizebe kukhala osangalala kwa moyo wawo wonse?​—Mla 9:9.

Kusonyezana chikondi ndi kumene kumachititsa kuti anthu akhale ndi banja losangalala. Anthu okwatirana ayenera kumatengera chitsanzo cha Isaki ndi Rabeka. Baibulo limatiuza kuti atakhala m’banja kwa zaka zoposa 30, iwo ankapitirizabe kukondana kwambiri. (Ge 26:8) Kodi mwamuna ndi mkazi wake angatani kuti nawonso azikondana chonchi?

Onerani VIDIYO yakuti Mungatani Kuti Banja Lanu Lizisangalala?: Muzisonyezana Chikondi. Kenako funsani omvera mafunso otsatirawa:

  • Kodi n’chiyani chingachititse kuti mwamuna ndi mkazi wake asamakondane kwambiri?

  • Kodi mwamuna ndi mkazi omwe ndi okwatirana angatani kuti aliyense azichititsa mnzake kumva kuti amamukonda komanso kumuganizira?​—Mac 20:35

8. Zofunika Pampingo

(5 min.)

9. Phunziro la Baibulo la Mpingo

(30 min.) bt mutu 10 ¶13-21

Mawu Omaliza (3 min.) | Nyimbo Na. 111 ndi Pemphero